Psalms 12

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide.

1Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;
okhulupirika akusowa pakati pa anthu.
2Aliyense amanamiza mʼbale wake;
ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.

3Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo
ndi pakamwa paliponse podzikuza.
4Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;
pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”

5“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu
ndi kubuwula kwa anthu osowa,
Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova,
“Ndidzawateteza kwa owazunza.”
6Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro
monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,
oyengedwa kasanu nʼkawiri.

7Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo
mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.
8Oyipa amangoyendayenda ponseponse
anthu akamayamikira zochita zawo.
Copyright information for NyaCCL